Ask AI
PrEP Implementation in Sub Saharan Africa
Kupanga Zofuna Motsogozedwa ndi Anthu a Kumudzi ngati Maziko a Ntchito ya PrEP ku Sub-Saharan Africa        

Released: March 26, 2026

Activity

Progress
1
Course Completed
Key Takeaways
  • Maphunziro a PrEP omwe amapangidwa ndi anzawo omwe amadziwa dera komanso omwe ali pa ziopsezo zofanana kawirikawiri amamvana bwino kuposa mauthenga a mabungwe okha.
  • Kutenga nawo mbali kwa anthu akumudzi pa kugwiritsa ntchito PrEP ndikofunikira kwambiri kuti anthu athe kupeza njira zodzitetezera ku HIV zokhazikika komanso zofanana.

Kuthekera kwa njira ya HIV pre-exposure prophylaxis (PrEP) yopewera HIV sikunazindikiridwe mokwanira m'madera ambiri a ku sub-Sahara Africa. Ngakhale kuti kugwira bwino ntchito kwa PrEP kuli m’kaundula wabwino, kusiyana pakati pa kupezeka kwake ndi kugwiritsidwa bwino ntchito kwake kukusonyeza mfundo yofunika kwambiri: Kugwiritsa ntchito bwino PrEP sikudalira kupezeka kwa mankhwala kokha komanso chidwi chochokera kumadera omwe akhudzidwa kwambiri ndi kachilombo ka HIV.

Umboni ochokera ku kafukufuku waposachedwapa wa ku Africa ukusonyeza kuti njira zotsogozedwa ndi anthu akumudzi pa kugwiritsa ntchito PrEP moyenera komanso kuchepetsa kusalana ndizofunikira kwambiri kuti ndondomekoyi ikhale yopambana.

Kugwiritsa Ntchito Magulu Odalirika Pobweretsa Chidwi
Njira zopambana zobweretsera chidwi zimagwiritsa ntchito malo ochezera omwe alipo kale komanso anthu odalirika akudera, m'malo mongodalira mauthenga ofalitsidwa kuchipatala kokha. Mu dera la asodzi la ku Uganda lomwe ali ndi kachilombo ka HIV, uphungu wa ogwira ntchito zachipatala komanso kuyankhulana ndi anthu mowakopa kudalimbikitsa anthu kuti azigwiritsa bwino ntchito PrEP ndi 86%.

Pamene mauthenga opewa kufala akuperekedwa ndi anzawo omwe amadziwa bwino deralo komanso ali  pa ziopsezo zofanana, amamvana bwino kwambiri kuposa mauthenga a mabungwe okha. M’boma la Mazowe ku Zimbabwe, kuphunzitsa atsikana achichepere kukhala akazembe a PrEP kudapangitsa kuti chiwerengero cha atsikana achisodzera ndi amayi achichepere omwe akutenga PrEP chiwonjezereke ndi 59% m'miyezi 7.

Mabwalo omwe anthu amakambirana zinthu akudera, monga magulu a ulangizi komanso zochitika za kudera, amagwira ntchito ngati malo abwino okambirana ndi kuthana ndi mabodza pamene akungoyamba. Ku Uganda, misonkhano ya ku dera yomwe idapangidwa kuti ithetse nthano zabodza, pophatikiza othandizira kutsatira osankhidwa kuchokera ku magulu am’chezo a anthu omwe amagwiritsa ntchito PrEP, idaonjezera kukakamira kugwiritsa ntchito PrEP kuchoka pa 6.7% kufika pa 47.9%.

Izi zikuwonetsa momwe magulu othandizira otsogozedwa ndi anthu a ku dera angasinthire bwino chidziwitso cha PrEP kukhala kutenga nawo mbali kokhazikika popewa HIV.

Kukhazikika pa PrEP Pochepetsa Kusalana
Kusalidwa kosalekeza kwa milingo yosiyanasiyana ndi chotchinga chachikulu pa kugwiritsa ntchito PrEP m'madera onse aku Africa. Anthu omwe angapindule ndi PrEP amaopa kuonedwa kuti ali ndi kachilombo ka HIV, kuweruzidwa chifukwa cha zikhalidwe zawo zogonana, kapena kuchitiridwa tsankho m'zipatala, zomwe zimawabwezera m’mbuyo kugwiritsa ntchito zithandizo za umoyo zokhazikika.

Kuvomereza njira motsogozedwa ndi anthu a ku dera cholinga chake ndi kuthana ndi mavutowa posintha kaonedwe ka PrEP ngati njira yokhazikika, yopereka mphamvu kupanga zisankho za umoyo osati thandizo losalidwa. Makalabu othandiza anzawo ndi magulu olimbikitsa anthu amapanga malo otetezeka kuti anthu azikambirana za PrEP poyera, kugawana zomwe amakumana nazo, komanso kubweretsa pamodzi kulimbika polimbana ndi kusalidwa. Amapereka luso kwa otenga mbali loti aziwulula momwe alili komanso kuthana ndi zokamba za anthu, zomwe zimagwirizana ndi kutsatira bwino ndondomeko za mankhwala.

Kuzolowera kumaphatikizapo kumvetsetsa zosowa zosiyana za anthu a ku dera, amene nthawi zambiri amafuna njira zoperekera thandizo zabwino komanso njira zosiyanasiyana zoperekera chithandizo zomwe zimalemekeza kufunika kwawo kwa chinsinsi. Kupereka mauthenga abwino, olunjika pa umoyo mosadukiza kudzera m'njira zosiyanasiyana, monga zochitika za anthu a ku dera, kufikira anthu paokha, ndi zithandizo zachikwanekwane zaumoyo zaubereki komanso uchembere wabwino, kungathandize kusintha manong’onong’o kuchoka pa mantha komanso kusalana kufika ku mphamvu ndi kupewa. Anthu akudera akamaona ogwiritsa ntchito PrEP ngati anthu osamala za umoyo wawo, anthu odalirika omwe amaika patsogolo thanzi lawo, kugwiritsa ntchito komanso kukakamira kugwiritsabe ntchito kwawo kumawonjezereka.

Madera monga Othandizana nawo pa Kupambana kwa Kupewa
Ulendo wa ntchito yopambana ya PrEP ku Africa maziko ake ali ndi anthu m'madera awo a eni akewo. Njira zobweretsera chidwi ziyenera kugwiritsa ntchito atsogoleri a ku dera, kupanga malo otetezeka okambirana momasuka, kupereka chithandizo chochokera kwa anzawo, ndikuwonetsetsa kuti pali njira zoperekera thandizo mwanzeru komanso mwaulemu.

Kafukufuku akusonyeza kuti pamene madera akutenga nawo mbali monga opanga nawo mapulogalamu opewera matenda m'malo mokhala ongolandira, kusalana kumachepa, kudalirana kumakhazikitsidwa, ndipo PrEP imasintha kuchoka ku chithandizo chamankhwala kukhala chida chokhazikika, chosavuta kugwiritsa ntchito pa umoyo komanso choperekera mphamvu. Chomcho, kuyika ndalama mu ntchito zopezera chidwi zoyendetsedwa ndi anthu a ku dera ndi kofunika kwambiri powonetstsa kuti ntchito zopewera HIV ndizokhalitsa komanso zofanana m’chigawo chonse.

Maganizo Anu
Ndi zitsanzo ziti za chidwi chakagwiritsidwe ntchito ka PrEP zomwe zimatsogoleredwa ndi anthu akumudzi zomwe mwaziona m'machitidwe anu? Kodi mungasinthe bwanji zitsanzo zomwe zafotokozedwa mu ndemangayi zokhudza kugwiritsa ntchito PrEP m’dera lanu? Perekani ndemanga kuti mulowe nawo mu zokambirana!