Ask AI
PrEP wa Aliyense
M'gwirizano wa PrEP wa aliyense: Chisankho Choyenera

Released: December 04, 2025

Activity

Progress
1
Course Completed
Key Takeaways
  • Kukambirana zokhudza PrEP molunjika HIV kumapangitsa kuti zokhudza PrEP zisalabadiridwe ndipo izi sizipereka mwayi kwa omwe akadatha kugwiritsa ntchito njirazi omwe amatha kudziona ngati sakupanga makhalidwe oyika “pachiswe” moyo wawo.
  • Kuthandiza anthu kuti asankhe PrEP molingana ndi zosowa komanso zokhumba zawo ndikuwapatsa mphamvu, osati kuwasala, ndipo izi zimapititsa patsogolo mchitidwe ogwiritsa ntchito PrEP komanso kulimbikira.

Kufika kwa mankhwala ozitetezera ku kachilombo ka HIV a pre-exposure prophylaxis (PrEP)kwathandizira kupewa kachilomboka Ikagwiritsidwa ntchito mosadukiza komanso pa mlingo wake, PrEP ili ndikuthekera kogonjetseratu mulili wa HIV kudzera mukuchepetsedwa kwa kufala kwa HIV. Komabe, sizokwanira kupereka mankhwala a PrEP kwa anthu okhawo omwe "ali pa chiopsezo."

Kafukufuku wa ku Africa, kumene nthendayi kwambiri simvetsetsekabe, adaonetsa kuti kugwiritsa ntchito chiopsezo ngati njira pounika kuvomerezeka kwa PrEP kumachepetsa kuthekera kwa zotsatira. Sizipereka mwayi kwa a mbiri amene akadatha kupindula, ndipo ili ndi kuthekera konyazitsa PrEP. 

Kafukufukuyu adaonetsa kuti m’madela amene HIV ndiyochuluka kwambiri komanso kuchepetsa chiwerengero cha tizilombo ta HIV si kwa aliyense (kusonyeza kupatsirana kwa tizilombo), chiwerengero chachikulu cha kufala kwa HIV chimachepetsedwa pomwe PrEP yaperekedwa kwa onse omwe angapindule. Kuthandiza kwake kumadalira kufikirika kwake, kugwiritsa ntchito, kagwiritsidwe ntchito kobweretsa zotsatira, komanso kulimbikira.

Tingatani kuti izi zitheke? Ndikukhulupilira kuti uchembere wabwino ndi gawo lofunika kwambiri pa umoyo wabwino. Pamene tikukumana ndi munthu amene ali pa msinkhu ochita zogonana, tifufuze ngati kuli kofunika kukambapo za kupewa. Anthu amene angaonetse chidwi chofuna PrEP akhoza kuphunzitsidwa za njira zomwe zilipo kuti asankhe iliyonse yomwe ndiyowakomera. Tili ndi njira zingapo za PrEP zomwe ndikuphatikizapo PrEP wakumwa, mphete yam'chiberekero, komanso mitundu 2 ya PrEP obaya Njira iliyonse ili ndi mapangidwe ake osiyana, kuphatikizapo kachitidwe kake komanso nthawi yogwiritsira ntchito.

Popanga kafukufuku wathu, pepala la lokhala ndi uphungu limaperekedwa, zomwe zimthandizidwanso ndi mabuku ena komanso zipangizo zamakono zomwe zimapereka uthenga owonjezera, kuunikira kuyipa komanso ubwino ndikuthandiza omwe angagwiritse ntchito PrEP kudziwa zokonda zawo asanakumane ndi akatswiri awo achipatala. Kenako uthengawu umaunikidwa ndi a HCP kapena achipatala awo poyang’ana ngati ndi ovomerezeka ndi achipatala molingana ndi njira zosiyanasiyana za PrEP, kuti ayambe kupereka PrEP.

Ubwino wa Kusankha
Zotsatira za ku M’mawa kwa Africa zidaonetsa ubwino operekea njira za PrEP kwa anthu zomwe zimagwirizana ndi zokhumba za aliyense. Ofufuza adapatsa ochita nawo kafukufuku kusankha pakati pa PrEP obaya, PrEP wakumwa, komanso ogwiritsa ntchito akangomaliza kugonana, ndi mwayi osankha kusintha pakutha kwa nthawi (KAFUKUFUKU osintha chisankho chopewera). Adapeza kuti kupereka mwayi osankha kudapangitsa kuti nthawi yogonana pogworotsa ntchito njira zachipatala idakwera kufika pafupifupi anthu makumi asanu ndi awiri 69.7%, kuyerekeza ndi 13.3% ya omwe amagwiritsa ntchito njira zawamba zopewera HIV. Zidathandizanso kuchepetsa kutenga HIV kufika pa (ziro) 0% kuyerekeza ndi pafupifupi anthu awiri 1.8% pa anthu zana alionse ogwiritsa ntchito njira wamba zopewera.

Taphunziranso mfundo zina zofunika mu ntchito yathu ya PrEP m’madela amene kuli anthu osauka, komanso okumana ndi zovuta zina ku Cape Town.

  1. Kupereka mwayi osankha kumatheka m’magulu operekera uphungu komwe timaphatikizanso njira zamsangulutso zodziyesa wekha kuti tidziwe zokonda Kusankha uphungu kungakhale ndi zotsatira zabwino pamene waperekedwa ndi aphungu ophunzitsidwa bwino otsogozedwa ndi mzamba kutsogolera kuyesa komaliza pofuna kuonetsetsa kuti HIV isakhalepo. Mu ntchito yathu, tidapereka LA CAB, mphete ya m'chiberekero, komanso PrEP wakumwa. Achinyamata ambiri azaka 16-29 adasankha PrEP obaya, ndipo ochepa kwambiri adasanga mphete ya m'chiberekero. Zifukwa zenizeni zidali kuganizira moyo wawo poyang’ana kwambiri ubwino moyerekeza ndi zovuta zake komanso ubwino wake.
  2. Chisankho chimasintha, osati pakapita nthawi yaitali pokha komanso ngakhale mukanthawi kochepa. Tidapeza kuti patapita masabata ochepa chabe, anthu adasintha kuchoka ku PrEP wakumwa ndi kuyamba kufuna wobaya, mosakaika adali ataona kuti PrEP idali yosavuta.
  3. Chisankho chimachulukitsa anthu ogwiritsa ntchito komanso kafikiridwe. Ku South Africa, taonetsa kuti kuonjezera zisankho za PrEP kwapititsa patsogolo kagwiritsidwe ntchito ka PrEP ngati njira yopewera.
  4. Kusankha kumabweretsa kulimbika kwabwino: pamene anthu atsimikizika pa chisankho chawo, amakhala olimba mtima ndi PrEP amene asankha.
  5. Njira zamakono zikhoza kulimbikitsa kupanga chisankho ndikuchepetsa chipsinjo pa aphungu komanso azamba.
  6. Pakhoza kukhala zovuta zina zobwera ndi njira zoperekera. Mwachitsanzo, ogwiritsa ntchito PrEP amene akufunadi kudziwa komanso chinsinsi akhoza kusankha PrEP wakumwa kapena mphete, zomwe zingaperekedwe pamalo obisika, osati kupita kuchipatala kapena malo ena omwe opezako thandizo kuti akabayidwe, yomwe ikuyenera kuperekedwa ndi achipatala kapena a HCP. 

Kukambirana zokhudza PrEP molunjika HIV kumapangitsa kuti zokhudza PrEP zisalabadiridwe ndipo izi sizipereka mwayi kwa omwe akadatha kugwiritsa ntchito njirazi omwe amatha kudziona ngati sakupanga makhalidwe oyika “pachiopsezo” moyo wawo. Mmalo mwake, achipatala kapena a HCP afotokozere za PrEP ngati njira ina iliyonse ya umoyo yopewera Kuthandiza anthu kuti asankhe molingana ndi zofuna zawo komanso makonda kuli ngati kuwapatsa mphamvu, osati kuwasala. Motero, kugwirizana pa nkhani ya PrEP kwa aliyense, motengera pa zokonda komanso chisankho cha aliyense osati chiopsezo, ndi zofunika kwambiri pofuna kubweretsa zotsatira zoyenera pa mulili wa HIV. 

Maganizo Anu
Mumayambitsa bwanji zokambirana zokhudza PrEP mu machitidwe anu? Mukuganiza kuti njira yabwino ndi iti pokambirana za PrEP ndi munthu amene akuganiza kuti sakufunikira izi? Perekani ndemanga kuti mulowe nawo mu zokambirana!